[1] Yesu anati kwa ophunzira ake,“Zinthu zimene zimachimwitsa sizingalephere kubwera, koma tsoka kwa munthu wozibweretsayo.
[2] Kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala wamphero mʼkhosi mwake kusiyana kuti achimwitse mmodzi mwa ana aangʼonowa.
[3] Nʼchifukwa chake dziyangʼanireni nokha. “Ngati mʼbale wanu achimwa, mudzudzuleni, ndipo ngati alapa, mukhululukireni.
[4] Ngati iye akulakwira kasanu ndi kawiri pa tsiku, ndipo ngati nʼkubweranso kwa iwe kasanu ndi kawiri nati, ‘Ndalapa,’ umukhululukire.”
[5] Atumwiwo anati kwa Ambuye, “Kulitsani chikhulupiriro chathu!”
[6] Yesu anayankha kuti,“Ngati muli ndi chikhulupiriro chachingʼono ngati kambewu kampiru, mukhoza kulamula mtengo wamkuyu uwu kuti, ‘Zulidwa ndi kukadzalidwa mʼnyanja,’ ndipo udzakumverani.
[7] “Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu anali ndi wantchito wolima kapena woweta nkhosa, kodi angawuze wantchitoyo atabwera ku munda kuti, ‘Tsopano bwera kuno khala pansi kuti udye?’
[8] Kodi sangamuwuze kuti, ‘Konzere chakudya cha madzulo, iweyo ukonzeke ndipo undidikirire pamene ndikudya ndi kumwa; kenaka ukhoza kudya ndi kumwa?’
[9] Kodi iye angathokoze wantchitoyo chifukwa chochita chimene anawuzidwa kuchita?
[10] Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munawuzidwa, muzinena kuti, ‘Ndife antchito osayenera; tangogwira ntchito yathu basi.’ ”
[11] Tsopano Yesu anayenda mʼmalire a pakati pa Samariya ndi Galileya pa ulendo wake wa ku Yerusalemu.
[12] Akulowa mʼmudzi wina, amuna khumi amene anali ndi khate anakumana naye. Iwo anayima patali
[13] ndipo anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Yesu, Ambuye, tichitireni chifundo!”
[14] Iye atawaona, anati,“Pitani kadzionetseni nokha kwa ansembe.” Ndipo pamene iwo ankapita, anachiritsidwa.
[15] Mmodzi wa iwo, ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, nayamika Mulungu ndi mawu okweza.
[16] Anagwetsa nkhope yake nagwa pa mapazi a Yesu ndi kumuthokoza. Ndipo iye anali Msamariya.
[17] Yesu anafunsa kuti,“Kodi amene anachiritsidwa sanalipo khumi? Nanga asanu ndi anayi ena ali kuti?
[18] Kodi palibe mmodzi mwa iwo amene anabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatula mlendoyu?”
[19] Pamenepo anati kwa iye,“Imirira ndipo pita; chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe.”
[20] Ndipo Afarisi atamufunsa Iye kuti, ufumu wa Mulungu udzabwera liti, Yesu anayankha kuti,“Mulungu sakhazikitsa ufumu wake mooneka ndi maso,
[21] kapenanso kuti anthu adzati, ‘Uwu uli apa,’ kapena ‘Uwo uli apo,’ Pakuti taonani ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”
[22] Kenaka Iye anati kwa ophunzira ake,“Masiku akubwera pamene inu mudzalakalaka mutaona tsiku limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona.
[23] Anthu adzakuwuzani kuti, ‘Uyo ali apoyo!’ kapena ‘Uyu ali apa!’ Musawathamangire iwo.
[24] Pakuti monga mphenzi ingʼanima ndi kuwala kuchokera mbali ina ya thambo kufikira inzake, koteronso adzakhala ali Mwana wa Munthu pa tsiku lake.
[25] Koma poyamba ayenera kuzunzika mu zambiri ndi kukanidwa ndi mʼbado uno.
[26] “Monga mmene zinkachitikira nthawi ya Nowa, momwemonso zidzachitikanso nthawi ya Mwana wa Munthu.
[27] Anthu ankadya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo. Pomwepo chigumula chinafika ndi kuwawononga onsewo.
[28] “Zinalinso chimodzimodzi nthawi ya Loti. Anthu ankadya ndi kumwa, kugula ndi kugulitsa, kudzala ndi kumanga.
[29] Koma tsiku limene Loti anachoka ku Sodomu, moto ndi sulufule zinavumbwa kuchokera kumwamba ndi kuwawononga onsewo.
[30] “Zidzakhalanso choncho Mwana wa Munthu akadzaonekera.
[31] Tsiku limenelo munthu amene ali pa denga la nyumba yake, ndi katundu wake ali mʼnyumbamo, asadzatsike kukatenga. Chimodzimodzinso, munthu amene adzakhale ali ku munda asadzabwerere kukatenga chilichonse.
[32] Kumbukirani mkazi wa Loti!
[33] Aliyense amene ayesetsa kusunga moyo wake adzawutaya, ndipo aliyense amene ataya moyo wake adzawusunga.
[34] Ine ndikukuwuzani inu, usiku umenewo anthu awiri adzagona pa mphasa imodzi; wina adzatengedwa ndipo wina adzasiyidwa.
[35] Amayi awiri adzakhala pamodzi akusinja; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa.
[36] Amuna awiri adzakhala akulima mʼmunda; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa.”
[37] Iwo anafunsa kuti, “Ambuye, kodi zimenezi zidzachitikira kuti?” Iye anayankha kuti,“Kumene kuli mtembo, nʼkumene makwangwala amasonkhanako.”