Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:36

[1] Efereimu amadya mpweya; tsiku lonse amasaka mphepo ya kummawa ndipo amachulukitsa mabodza ndi chiwawa. Amachita mgwirizano ndi Asiriya ndipo amatumiza mphatso za mafuta a olivi ku Igupto.

[2] Yehova akuyimba mlandu Yuda; Iye adzalanga Yakobo molingana ndi makhalidwe ake, adzamulanga molingana ndi ntchito zake.

[3] Akali mʼmimba mwa amayi ake, Yakobo anagwira chidendene cha mʼbale wake; iye atakula analimbana ndi Mulungu.

[4] Yakobo analimbana ndi mngelo ndipo anapambana; analira napempha kuti amukomere mtima. Mulungu anakumana naye ku Beteli ndipo anayankhula naye kumeneko,

[5] Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Yehova ndiye dzina lake lotchuka!

[6] Koma inu muyenera kubwerera kwa Mulungu wanu; pitirizani chikondi ndi chiweruzo cholungama, ndipo muzidikira Mulungu wanu nthawi zonse.

[7] Munthu wamalonda amagwiritsa ntchito masikelo achinyengo; iyeyo amakonda kubera anthu.

[8] Efereimu amadzitama ponena kuti, “Ndine wolemera kwambiri; ndili ndi chuma chambiri. Palibe amene angandiloze chala chifukwa cha kulemera kwanga.”

[9] “Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa mu Igupto. Ndidzakukhazikaninso mʼmatenti, monga munkachitira masiku aja pa nthawi ya zikondwerero zanu.

[10] Ndinayankhula ndi aneneri, ndinawaonetsa masomphenya ambiri, ndipo ndinawawuza mafanizo kudzera mwa iwo.”

[11] Kodi Giliyadi ndi woyipa? Anthu ake ndi achabechabe! Kodi amapereka nsembe za ngʼombe zazimuna ku Giligala? Maguwa awo ansembe adzakhala ngati milu ya miyala mʼmunda molimidwa.

[12] Yakobo anathawira ku dziko la Aramu, Israeli anagwira ntchito kuti apeze mkazi, ndipo anaweta nkhosa kuti akwatire mkaziyo.

[13] Yehova anagwiritsa ntchito mneneri kuti atulutse Israeli mu Igupto; kudzera mwa mneneriyo Iye anawasamalira.

[14] Koma Efereimu wamukwiyitsa kwambiri. Nʼchifukwa chake Yehova adzawalanga ndi imfa. Adzawalanga chifukwa anamuchititsa manyazi kwambiri.

Hoseya — Chapters