Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:25

[1] Pemphero la mneneri Habakuku potsata mayimbidwe a Sigionoti.

[2] Inu Yehova, ndamva za kutchuka kwanu; Inu Yehova, ntchito zanu zandiopsa. Muzichitenso masiku athu ano, masiku athu ano zidziwike; mu ukali wanu mukumbukire kuchita chifundo.

[3] Mulungu anabwera kuchokera ku Temani, Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani. q4 Sela Ulemerero wake unaphimba mlengalenga ndipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake.

[4] Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa; kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake, mʼmene anabisamo mphamvu zake.

[5] Patsogolo pake pankagwa mliri; nthenda yoopsa inkagwa kumbuyo kwake.

[6] Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi; anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera. Mapiri okhazikika anagumuka ndipo zitunda zakalekale zinatitimira. Njira zake ndi zachikhalire.

[7] Ndinaona matenti a ku Kusani ali pa mavuto, mokhala a ku Midiyani muli ululu waukulu.

[8] Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje? Kodi munakalipira timitsinje? Kodi munapsera mtima nyanja pamene munakwera pa akavalo anu ndiponso magaleta anu achipulumutso?

[9] Munasolola uta wanu mʼchimake, munayitanitsa mivi yambiri. q4 Sela Munagawa dziko lapansi ndi mitsinje;

[10] mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka. Madzi amphamvu anasefukira; nyanja yozama inakokoma ndipo mafunde ake anakwera kwambiri.

[11] Dzuwa ndi mwezi zinayima chilili mlengalenga, pa kungʼanima kwa mivi yanu yowulukayo, pa kunyezimira kwa mkondo wanu.

[12] Munayendayenda mʼdziko lapansi muli ndi ukali, ndipo munapondereza mitundu ya anthu muli ndi mkwiyo.

[13] Munapita kukalanditsa anthu anu, kukapulumutsa wodzozedwa wanu. Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa, munawononga anthu ake onse. q4 Sela

[14] Ndi mkondo wake womwe munalasa mtsogoleri wake pamene ankhondo ake anabwera mwamphamvu kudzatibalalitsa, ankasangalala ngati kuti akudzawononga osauka amene akubisala.

[15] Munapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu, kuvundula madzi amphamvu.

[16] Ndinamva ndipo mtima wanga unagunda kwambiri, milomo yanga inanjenjemera pakumva phokosolo; mafupa anga anaguluka, ndipo mawondo anga anawombana. Komabe ndikuyembekezera mofatsa, tsiku la masautso limene lidzafike pa mtundu wa anthu umene ukutithira nkhondo.

[17] Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa, ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa. Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso, ndipo mʼminda musatuluke kanthu. Ngakhale nkhosa ndi ngʼombe zithe mʼkhola,

[18] komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

[19] Ambuye Yehova ndiye mphamvu yanga; amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbawala yayikazi, amandithandiza kukafika pamwamba pa phiri. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za nsambo.

Habakuku — Chapters