[1] Pa za kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu ndiponso za kusonkhana kwathu kuti tikumane naye, abale, tikukupemphani
[2] kuti musagwedezeke msanga mʼmaganizo kapena kuopsezedwa ndi uneneri, mbiri kapena kalata yokhala ngati yachokera kwa ife, yonena kuti tsiku lija la Ambuye linafika kale.
[3] Musalole kuti wina aliyense akunamizeni mwa njira ina iliyonse. Pakuti tsikulo lisanafike, kudzakhala mpatuko waukulu kwambiri, ndipo kudzaoneka munthu woyipitsitsa uja, munthu woyenera kuwonongedwayo.
[4] Iyeyo adzatsutsa ndi kudziyika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza. Iyeyo adzadzikhazika mʼNyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.
[5] Kodi simukukumbukira kuti pamene ndinali nanu pamodzi ndinkakuwuzani zimenezi?
[6] Ndipo tsopano mukudziwa chimene chikumuletsa kuonekera, koma adzawululika pa nthawi yake yoyenera.
[7] Pakuti mphamvu yobisika yoyipitsitsa ikugwira ntchito ngakhale tsopano; koma amene akutchinga mphamvuyo adzapitiriza kutero mpaka pamene wotchingayo adzachotsedwe.
[8] Ndipo kenaka woyipitsitsayo adzaonekera, amene Ambuye Yesu adzamugonjetsa ndi mpweya otuluka mʼkamwa mwake ndi kumuwononga ndi ulemerero wa kubwera kwake.
[9] Woyipitsitsayo adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzaonetsa mphamvu zake pochita zizindikiro ndi zodabwitsa zachinyengo.
[10] Iye adzagwiritsa ntchito mtundu uliwonse wachinyengo kupusitsa amene akuwonongeka. Iwo akuwonongeka chifukwa akukana kukonda choonadi ndi kuti apulumutsidwe.
[11] Chifukwa cha chimenechi, Mulungu akuwatumizira chinyengo chachikulu kuti akhulupirire bodza.
[12] Choncho adzalangidwa onse amene sanakhulupirire choonadi, koma anakondwera mu zoyipa.
[13] Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu mʼchoonadi.
[14] Iye anakuyitanirani zimenezi kudzera mwa uthenga wathu wabwino, kuti mulandire nawo ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu.
[15] Kotero tsono, abale, imani mwamphamvu ndi kugwiritsa ziphunzitso zimene tinakupatsani kudzera mʼmawu apakamwa kapena kudzera mʼkalata.
[16] Ambuye athu Yesu Khristu mwini ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ife ndipo mwachisomo chake anatipatsa kulimba mtima kwamuyaya ndi chiyembekezo chabwino,
[17] akulimbikitseni ndi kukupatsani mphamvu yogwirira ntchito ndi kuyankhula zabwino zilizonse.