[1] Tsono abale, za nthawi ndi nyengo yake nʼkosafunikira kuti tikulembereni,
[2] chifukwa mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala usiku.
[3] Pamene anthu akunena kuti, “Mtendere ndi chitetezo,” chiwonongeko chidzafika pa iwo mwadzidzidzi, monga zowawa za amayi pobereka, ndipo sadzathawa.
[4] Koma inu abale, simuli mu mdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mbala.
[5] Nonse ndinu ana a kuwunika ndi ana a usana. Sindife anthu a usiku kapena mdima.
[6] Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga.
[7] Pakuti amene akugona, amagona usiku, ndi amene amaledzera, amaledzera usiku.
[8] Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa.
[9] Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
[10] Iye anatifera ndi cholinga chakuti, kaya tili ndi moyo kapena tagona, tikhale naye pamodzi.
[11] Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.
[12] Tsopano tikukupemphani abale kuti muziwalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene amakuyangʼanirani mwa Ambuye ndi amene amakulimbikitsani.
[13] Muziwachitira ulemu kwambiri mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo. Mukhale pa mtendere wina ndi mnzake.
[14] Ndipo tikukupemphani abale, muwachenjeze amene akungokhala osagwira ntchito, alimbikitseni amanyazi, thandizani ofowoka ndipo muzilezera mtima aliyense.
[15] Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse.
[16] Kondwerani nthawi zonse.
[17] Pempherani kosalekeza.
[18] Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.
[19] Musazimitse moto wa Mzimu Woyera.
[20] Musanyoze mawu a uneneri.
[21] Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino.
[22] Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse.
[23] Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu.
[24] Amene anakuyitanani ndi wokhulupirika ndipo Iye adzachita zimenezi.
[25] Abale, mutipempherere.
[26] Perekani moni wachikondi kwa onse.
[27] Pamaso pa Ambuye ndikulamula kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.
[28] Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale nanu.